Mark Chichewa sweet store's

Mark Chichewa sweet store's Just writing store

30/05/2022


Part (3) Wolemba Mark2

🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑

Musaiwale tikupitiliza nkhani yathu. mongokukuni,ma comments ani ndi ma like mdiamene amapeleka chilimbikiso kwa olembafe

Continue πŸ‘‡

Atamaliza kuyankhula mkaziyo ndinamufunsa k*ti ndiziwe chomwe amafuna k*ti ndimuthandize koma ndinazizimuka ndimau amene anandiyankha (ayini inetu ndimakhulupila k*ti mungathe kumusamala nkazi ndipo ndikuziwa k*ti mau angawa ndikupeleka kwa munthu oyenela)
Nditanva izi ndinazizimuka koma sindinafune kumuonesela. Mwachidule ndinamuyankha k*ti eya ndizoona koma mukuziwa Joseph ndi mzanga ok*ti tachoka k*tali ndie sindingamupange chipongwe. Koma ngati mukufuna ndikhoza kuk*thandizani pa vuto lomwe mulinayo ya kumuzi. Apatu chomwe mdikatanthauza ndimati ndimubweleke ndalama k*ti atumize kwao k*ti akazayambanso ntchito azandibwezele.

Koma chomwe anandiyankha anati ok mulimonsemo ayini inu ndi mamuna ine ndi mkazi ndie palibe chomwe chingavute. Mosakhalisa ndinalowa mnyumba kukatenga ndalama kumupasa k*ti akatumizile mayi ake mamuna wake asanabwele ndipo zinathekadi.

Mazulo k*tada ndinadabwa phokoso mkaziyo akulila nditayandikila pa chiseko ndimazindikila k*ti anali akumenyedwa ndi mamuna wake. Jose! Jose! Ndinaitana uku ndikugogoda chiseko atatuluka ndinamufunsa k*ti andiuze chomwe chimachitika koma palibe chomwe analankhula chonveka chifukwa anali atalezelelatu. Izitu zinandinvesa chisoni maka ndikaganizila sogolo ya nkaziyo.
Mosataya nthawi ndinabwelela m'room yanga kukagona. Mmawa k*tacha ndinanyamuka wa kuntchito mazulo nditaweluka ndinabwelela panyumba Nditafika ndinatenga 4n yanga koma ndinadabwa k*ti ndapangidwa Hi ku WhatsApp page yanga pa number yachilendo nditayang'anisisa pc anali nkazi yemweuja. Nditamuyankha tinayamba kucheza koma ndinadabwa mmene nkaziyu akamasukila. Anandiuza k*ti ayini mumandisangalasa oti ndimaganiza k*ti popanda inu ine ndikanavutika pano ndipo ndipo mutandipepha k*ti ndikuchitileni chilichonse ndikhoza kuchita.
Chifukwa cha machezedwe athu, mwa zizizi ndinazindikila ndagwa nae m chikondi nkaziyi ndipo malonjezo anayambika koma chomwe chikavuta ndi mpata ok*ti tikumane pa awili monga muziwa anthu oyandikana.

Komatu ngakhale ndikapanga izi ndinali okhuzika maka ndikaganizila komwe ndachoka ndi nzangai. Potengela mmene tikamasukilana ndi mzangao sikulina tili ku ntchito ndinamufunsa Joseph k*ti andiuze chichikuvuta mbanja mwake k*t asamagwilizane ndi mkazi wake koma ndinatutumuka atandiyankha k*ti

Wait part 4 ⚑⚑⚑⚑

27/05/2022


Part 2 by Mark2
🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑 🏑

Timalekeza Pok*ti, nkazi wa Joseph abwana ake anachoka kotelo anayamba amuimika kwa ma week angapo. zimene zinapangisa k*ti azikhala pakhomo.continue πŸ‘‡

Siku lina Saturday mmawa ndili chigonele mu room yanga ndinanva kugogoda pa chiseko changa.ine poesa ndi nzanga sindinavale mokwanila koma nditatuluka ndinadabw nkazi wa mzangayo ali pakhomo yanga.ndinatutumuka maka mmene ndinavalila monga muziwa munthu ukamachoka pogona, ndipo mosakhalisa ndinabwelela nyumba kukavala zovala zanga ndikuyamba kumulonjela nkaziyo.
Zinali motele. πŸ‘‡

Mwazuka bwanji mula?
Mmm mula bola kwacha.
Anayankha nkazi mosisitika nkhope atagwesa pansi ndinamuyang'ana koma ankaonekak*ti osausika pa chinachake.
Ndinamufunsa k*ti,
Mula vuto ndichani koma zikuenda?
Anayankha nkazi,mmm mula kunena mosanama kuenda palibe ndili mmavuto azaoneni moti sindikuziwa k*ti chikubwela kusosgolo kwanga ndichani.

Nditanva izi ndinali otutumuka mu mmtima moti sindimanvesa chimene mkaziyo ankatanthauzanji. Koma zinanditengela kanthawi k*ti ndimunvesese, kotelo ndinamufunsa k*ti achimwene alik*ti?
Koma anandiyankha k*ti sakuziwa komwe wapita amuna wake.
Ndinati ok. koma ndichani chakubwelesani mmawa ngati uno mula?
Nkazi anayamba kufotokoza motele.

Alamu ine ndakupezani.munthune ndili mmavuto azaoneni sindinkaziwa k*ti amuna anga ali motele koma paja amati Alidele nkulinga utaendanae
Munthune ndilindi ana awili onse aamuna oyamba bambo ake anamwalila pa ngozi ndili ndi mimba ya miyezi 6 kenako nditachila ndinanvana ndi Joseph za banja ndipo pachiyambi zimaenda bwino kwambili moti ndinabelekanso mwana wina wachiwiri uyo anali wa Joseph kenako anabwela kuno kundisiya ine kwathu pamozi ndi ana onse awiri
Kenako ndipamene anapanga zoti ndibwele kuno ndipo zinathekadi.

Masiku oyambilila zinkaenda inunso mumaona koma pano zinavuta amunanga sakupeleka chithandizo cha ana ngakhale ndikagwila ntchito ndalama amafuna ndiziwapasa azikamwela mowa ndi azinzao. pano kuntchito anandiimika iwo akugwila akulandila koma mnyumba mulibe chakudya ngakhale bread or softdrink tikuchita kuisowa moti pano angolawilapo mmawa limene sindiziwa k*ti apita k*ti pamene ine zulo ndalandila 4n kumuzi ak*ti amayi akudwala.ndie mmm ayini ndavutika.
Asanamalize nkazi misozi inayamba kusikila mmasaya mwake.

Kenako ndinamufunsa k*t ndie mula inu pondifotokozela nkhaniyi munali ndi cholinga chiti ndimufunse kapena ganizo linali yotani? Ikupitilila

Wait part 3 ⚑ ⚑

26/05/2022


Wolemba Mark 2

Pepani alembi chonde yesesani kundipangila post nkhani yangai ngakhale anthu page yanui samaikonda koma zimene zinandichitikila ndimafuna ena atengelepo phunzilo

Zina langa ndiine mavuto ku Malawi ndimachokela ku phalombe ndinabwela Kujoni kuno mu 2019 Ndinafikila kwa mchimwene wanga. Mosatenga masiku anadipezela ntchito kwa mzungu wina koma nchitoyo inali yokhalila komweko. Masiku oyambilila zimandivuta maka potengela chiyankhulo ndi zina komabe pang'ono ndi pang'ono ndinayamba kuzolowela.

Mwamwayi pantchitopo ndinapezapo mzanga,mmalawinoso zina lake Joseph yemwe ndikagwilizana naye kwambili moti timakhala ngati mchimwene wanga ndithu ankandilimbisa mtima monga muziwa mlendo komanso ziko laweni.

Patadusa chaka chimozi mzangayo anaitanisa nkazi wake kuchokela kumuzi (kumalawi) atafika tinamulandila kuena zoona anali nkazi ochezeka,opanda mwano, komanso wakhalidwe.koma ngakhale mzanga anaitanisa mkazi kucheza bwino ndiine sitinasiye mpaka nthawi zina ine zikawavuta kumbali ya ndalama ndimatha kuwathandiza maka potengela k*ti kuno ku joni munthu woti ali ndi banja kuno pena zinthu zimatha kumusokonekela ndie ine ndimatha kumupqsa ndalama k*ti athandizike.

Pakupita kwa masiku pang'ono ndi pang'ono nkazi uja anayamba kundizolowela nthawi zambili ndimaesesa kukhala mnyumba koma amatha kundiitana mamuna wake akachokapo tizicheza panja vuto limene tinalinayo ndiya ma room athu anali oyandikana kwambili choncho pena zimavuta k*ti ndibisale maka akamandiitana mkazi-yo.

Kenako mkaziyo anayamba ntchito kwa mzungu wina ndipo masiku oyambilila zinthu zimaenda ndithu koma patadusa miyezi ingapo zinthu zinayamba kuvuta maka nkazi akalandila ndalama kumakhala makangano chifukwa Joseph samafuna k*ti mkazi wakeyo azitumiza thandizo kumuzi kwa makolo ake vuto nzangayo anali wa chakumwa ndie nthawi zambili akalezela amabalalika moti olo pakhomo zimakhala zovutilapo k*ti athane ndi mavuto ena
Komanso ndalama ya nkazi akalandila amakonda kuimwelanso mowa.

Zinthu zinapitilila kusaenda mjanja mwa Joseph moti nthawi zina nkaziyo amandifotokozela mavuto ena amene akukumana nao m'banjamo koma ine ndimkangomulimbjisa ntima k*ti azingopemphela mwina mamuna wake azasintha. Kenako nkaziyo abwana ake anachoka kotelo anayamba amuimika kwa ma week angapo zimene zinapangisa k*ti azikhala pakhomo.

Dikilani part 2 k*ti munve k*t zinatha bwanji koma ndik*ti nkhani iyi ndiyosekesa komanso yodandaulisa
Ingoponyani comments k*ti zisakuphonyeni⚑⚑⚑

Hello people
23/05/2022

Hello people

28/04/2022

{2}


πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄

Salome asanamuyankhe Jeffrey anakumbukila mau amene agogo ake anamuuza ak*ti mamuna wabwino salembedwa pa mphumi apatu salome anatanganidwa ndi maganizo maka poziwa k*ti ali ndi nzake okondeka Joyce.kodi joy akaziwa k*ti ndapanga izi sanditenga kukhala opepela?
Nanga mamunai ndikamulola lelo ndi lalo samaesa k*ti ine ndi hule?
Nanga ndikamukana sindiluza mwayi wanga?

Kotelo salome zinamutengela nthawi k*ti apeze njila yomuthandiza kenako Jeffrey anamufunsa salome ngati ali ndi phone k*t amupase number ndicholinga aziimbilana apatu salome sanachedwe koma kupeleka # yake kwa Jeffrey Atatelo awiliwa anagwilizana k*ti aimbilana mazulo k*t apitilize pomwe analekezela Atatelo salome sanatenge nthawi koma kusazika kumapitiliza ulendo wake.

Ananyamuka salome anaesa kuenda mothamanga k*ti amupeze Joyce komavayi sizinathandize kanthu poti nae joy mayendedwe ake sanali aja ak*ti mmbuyo wasiya munthu ayi koma ngati waipidwa ndi chinthu chinachake

Salome atafuka ku msika anaesa kumufufuza Joyce koma sanapezele mosataya nthawi salome anaganiza zobwelela kunyumba. asanafike kwao anaganiza zozela kwawo kwa Joyce k*ti akamuone ngati wafika.apatu Joyce anali atafika kale kwao koma ali oyipidwa ndi zomwe anachita salome poima ndi nyamata yemwe samaoneka bwino kwaiye.

Odii Odii salome anaodika uku aku akusendela kukhomo joy atanva k*ti salome wafika anatuluka kuchipinda kwake komwe anali kuyamba kuseka monyogodola anvekele πŸ‘‡
Mmh asikana ameneo e-e anzathu zikuenda! Koma ine mpaka kusiidwa ndekha kumapita inu mutaima ndi nyamata, Nyamata-yonso kukhala osaonekabwilo ngati ameneuja? Asikana polani moto πŸ”₯πŸ”₯ ndie ak*ti kwao ndik*ti amula aja?
Salome atanva izi sanayankhe kanthu anangoti joy ndapita kobwela kwanga ndimaesa ngati ndikuzamuona nzaga ngati wafika bwino sindinabwele kuzayabana ndi munthu ayi.
Mosakhalisa salome ananyamuka ulendo kumapita kwao
Mazulo salome atamaliza kugwila ntchito zapakhomo analowa kuchipinda chake kukagona atangofika Jeffrey anaimba 4n πŸ“²
Salome πŸ“ž Hello
Jeffrey πŸ“žHello salome wafika bwanji?
Salome πŸ“žndafika bwino kwambili kaya inu mwafika bwanji
Jeffrey πŸ“žinenso ndafika bwino kwambili koma mosataya nthawi ndimafuna ndiziwe k*ti wahaniza motani ndi mfundo yathu ija imene tikakambilana mamawa
Salome πŸ“ža-a-aa kungoti ndiine mwana aa koma makolo anga ndiovuta

Awiliwa anapitiliza kukambilana pa 4n mpaka salome anavumela

wait part 3 is waiting your comment

26/04/2022



Writing by Mark Phiri

πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”΅πŸ”΄πŸ”»

Pamuzi wina panali asikana awili okondana kwambili (Joyce ndi salome) asakanawa ankakonda kuendela limozi nthawi zambili moti sipakadusa tsiku asanakumane.makolo ayo anali osangalala kamba ka kucheza kwa anawa.
Nthawi zambili asikanawa amakonda kuendela limozi ngati kunsika,kuchigayo, kuchalichi ndi kwina kulikonse komwe iwo angafune.
Komatu ngakhale Zinali chomwechi asikanawa analo ndi zokhumba zawo maka pa nkhani za chikondiπŸ’“ aliyense akafasa amamuuza mzache mamuna yemwe akumufuna pa umoyo wake.
Joyce ankati mamuna amene akufuna asakhale osauka chifukwa sakufuna azizazunzika m'banja
Pomwe salome amati iye sangasankhe mamuna chifukwa mdaliso umene mulungu wamupangila sakuuziwa izitu zinapangisa asikanawa kusiyana maganizo chifukwa Joyce samafuna kukhla ophweka kwa anyamata ammuzi ati chifukwa ndiosauka koma a m town.

Tsiku lina asikanawa anyamuka ulendo ku msika. alinkati mwanjila anakumana ndi nyamata wina akuenda pansi koma atavala silipasi imozi ina ili mmanja koma yoduka kachingwe kamozi Joyce atamuona nyamatayi anayamba kunyogodola anvekele mm amuna enawa alibe chochita kungokhala amuna ndik*tha choncho aziti akukufuna heee
Koma salome sanayankhe kanthu
Kenako asikanawa anakumana ndi nyamatayo apatu nyamatauja anaima nayambakupelwka moni kwa asikana aja koma Joyce mmalo moti avomele moni pokhla k*ti anali kusogolo kwa mzake zinamvuta mmalo mwake anangosusa vu! Kumusiya salome ali chiimile ndi nyamata uja ataenda pang'ono Joyce anayang'ana mmbuyo koma anadabwa k*t mzache sakubwela apatu joy anayamba kuzinenela anvekele (mh anthu ena amafuna kuzitchipisa ndithu koma munthu alili muja ndiok*ti akakuimise! Ine ndie ayi sindingapange zibwanazo)
Tione za salome πŸ‘‡
Salome Atakumana ndi nyamata uja zinawatengela ka nthawi akungoyang'anizana koma osayankhulana kenako nyamata uja anapeleka moni Mulibwanji sister?
Mwamanyazi salome anayankha.
INE ndine Jeffrey ndimakhala kusidya ukooo koma pano ndikupita pantundapo ndikukamuona nzanga choncho pa kukumana ndiinu ndachiesa chamwayi.
Salome=mwayi wake wanji?
Jeffrey= sister ndakukondani tikhale mchikondi
Salome atanva izi anafuna k*ti anyamukepo koma Jeffrey anamutchingila kusogolo.
Sorry ndili pa changu ndiloleni ndipite natelo salome.
Koma Jeffrey anati zoonadi ndikuziwa koma ukachoka usanandiyankhe ndiziwa bwanji maganizo ako? Apatu salome anakumbukila mau amene agogo ake anamooza ak*ti mamuna wabwino salembedwa..... wait part 2

06/04/2022

Hello people mwaswela bwanji

02/12/2021

(1)



πŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’Ž

Natasha anali msikana wokongola wamakhalidwe komanso onvela makolo ngakhale makolo ake anali osauka kuma iye sanagwe mmaeselo monga asikana anzake omwe amagulisa thupi lao ndi ndalama. Koma maloto a Natasha ankafuna atazakhala ndi banja losangalala ndi mamuna omukonda komaso omunvesesa.

Siku lina Natasha ndi azinzake ali pa mjigo busy k*tunga mazi ananva huta ya galimoto po-po-po atayang'ana anaona galimoto ina ikudusa koma mwa pang'ono pang'ono atayang'anisisa anaona nyamata wina yemwe amkamukodula Natasha k*t apite Natasha atasendela pafupi Zinali motele ‡‡

Hi zabhobho? Natasha anavomela Kona mwamantha chifukwa anali asakuziwa k*t akucheza ndi ndani.
(Bhobho!)
Ok ine ndi Jordan ndimakhala ku town ya Blantyre koma pano ndikupita kwa uncle anga pamunsipo ndie nditakuona ndakopeka ndi maonekedwe ako kotelo ndalephela kuugwila ntima ndipamene ndachiona chopambana k*ti ndikambulanenawe mkazi

Natasha atanva izi anagwidwa ndi mantha chifukwa cha moyo wachimizi zinamuvuta muntima k*ti amulole Jordan kotelo Natasha anayankha nati pepani achimwene mawu amene mwanena ndawanva koma sorry sindingakhale pa banja ndi munthu amene sindikumuziwa Jordan atanva izi sanapite patali anati ok chabwino koma ungandiuze zinalako?
Natasha anapeleka zina kwa Jordan ndipo mosakhalisa Jordan analiza galimoto yake kumapitiliza ulendo wake.
Atafika Jordan kwa amalume ake anayamba kuwafufuza uncle ake mbili ya Natasha ndipo uncle ake anamuuza khalidwe lonse ya Natasha apatu sanapite patali koma kuwapempha k*ti akamufunsilila Natasha.
Mosachedwa uncle anapanga dongosolo lachidule pokambilana ndi makolo ake anatasha mosakhalisa omwe anamuuza mwana wawo k*ti asautaye mwayi ndipo izi zinathekadi Natasha anakwatilana ndi Jordan namutenga kupita m town.

Awiliwa anaiyamba banja lao mosangalala ndipo osanama Jordan anali nyamata oziwa kusamala banja ok*ti Natasha anali osangalala k*ti maloto ake akwanisidwa.
Koma Jordan atakhala anaona k*t asafulumile kukhala ndi mwana ndi cholinga k*ti akonzekele bwino zofunika ngati banja la newone atakhala pansi ndi nkazi wake kumufotokozela Natasha sanavute anavomela zomwe mamuna wake anamupempha kotelo awiliwa amagwilisa nchito family-plan k*ti asakhale ndi mwana mwachangu.

Koma pang'ono ndi pang'ono Natasha anayamba kuchapika zimene zinapangisa k*ti ayambe kuiwala ntchito yake ngati mayi wapakhomo anayamba mwano...

28/11/2021

I miss my fans πŸ€πŸ€

12/11/2021

(6)

πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”

Choyamba ndipepese chifukwa chosapitiliza nkhaniyi masiku apitawa izi zachitika chifukwa cha 4n inaonongeka koma pano chilichonse chili bwino ndithu.
Tipitilize πŸ‘‡ πŸ‘‡

Moses atamaliza kuyankhula Emily anamukumbatila moses anati ngati ukunena zoona k*ti supitilizana ndi sofiya ndakukhulukila koma ndisazanvenso kachikena please ndikuona ngati ndizosaenela k*ti ndizilandizana mamuna ndi nzanga Ndipo moses anati,,, ndikulonjeza suzaonanso zimenezi
Apatu Emily sanapitilile ulendo opita kwa sofiya anangobwelela pomwepo kumapita kunyumba.

Sofiya atakhala anaganiza k*ti akamuone moses. Atafika ku trading anamupeza mozy akuenda bawo ndi azinzake atamuitana moses anapita monyinyilika atafika pomwe pamali sofiya moses anangofikila funso
Eya umatibwanji?
Sofiya::mozy bas kufuna kundipusisa ine eti! Umakatani kumenekuja ndi Emily nzanga weni weni?
Moses anamuyankha naati: Sofiya ndikuuze chilungamo ine sindinafune iwe ndinafuna Emily ndie kumbukila k*ti unachita kulanda ndie ndie usandisokoselepo apo bas kasake ena iwe ndi ine tathana.
Sofiya ak*ti ayankhule moses anangonyamukapo ulendo pabawo sofiya anangoti lakasi misozi ikulenga mmaso kenako anauyamba ulendo obwelela kunyumba.

Patadusa mwezi umozi(1) sofiya anadabwa k*ti wayamba mwezi wina koma osaoloka msinje komanso nthawi zina amatha kuona chizungulile ngati afuna kugwa, pena amaona mselu pena osafuna chakudya Apatu sofiya anaziwa k*ti sizili bwino koma maganizo amabwela k*ti akamuuze mozy za mimba yake koma pena amazisusa k*ti mmene anandipangila sikulija ndie ndikamuuze za mimba akalola?
Patatha myezi iwili (2) Sofiya analimba ntima k*ti akamuuze mozy za mimba yake Ndipo ananyamukanso kupita ku trading poti ndi kumene moses akapezeka kawili kawili ndie akamufuna akangopita komweko.
Atafika anamupeza mozy akusuka matumbo ambozi monga nchito yake kenako moses anamufunsa sofiya k*ti,, wabwelanso ndi zotani lelo? Sofiya anati ndimafuna tikambilane pambali please ngati zingatheke.
Awiliwa anakokelana kuseli kwa shop ina atafika moses anati,, eya umatibwanji?
Sofiya> Ndimafuna ndikuziwise k*ti sindilibwino
Moses> ukudwala chani?
Sofiya> palibe koma ndili ndi mimba.
Moses anayamba kuseka πŸ˜‚ πŸ˜‚ kenako anafunsa,, yamezi Ingati?
Sofiya> mezi iwili, nanga bwanji ukuseka?
Moses> ndikuseka chifukwa iwe ndi munthu osanva, ndinakuuza k*ti tathana ndie ukubwela ndi mau oti ulindi mimba ukuona ngati ungandipusise ine? wait part. 7

03/11/2021

(5)

πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”

Mozy atalandila 4n mutu unamuima chifukwa panthawiyi anali ndi Emily komweko ndie zinamukoka manja k*ti angapange bwanji k*ti akaziwa asakumane. Apatu moses anaganiza k*ti agwilise ntchito plan (B) Zinali motele.moses anatuluka panja kumusiya Emily nkati momwemo, anaimba 4n πŸ“² kwa Sofiya kumuuza k*ti iye saali ku meneko ali k*tali ndi delalo ndie amudikila after 3hours ⌚ akhala atafika Koma πŸ‘ƒ mphuno salota Nthawi imene sofiya ankaimba 4n πŸ“± anali atafika kale moti ganizo lake inali lak*ti mozy akamupeza komweko. Sofiya anamuuza mozy pa 4n πŸ“± k*ti wafikakale nthawi yomweyo maso anangoti gululu kukumana.(Honney bwanji umakonda zondiesa k*teloko unali utafika kale?) uyutu anali sofiya kumufunsa mozy koma mozy anangoti kakasi kusowa choyankha.nae Emily atanva mau asofiya anazuka pa bed kuyambakuzifunsa k*ti sofiya akuzatani kuno? Sofiya anangoti Street kulowa nkati apatu sofiya anatutumuka atampeza Emily ali chiimile wavala zamkato zokha

Emily uk*tani muno? Uyu anali sofiya kumufunsa Emily uku akuoneka odabwa kwambili Emily: ine ndiamene ndikuenela kukufunsa k*ti ukufuna chani kuno?
Sofiya anayamba kulila uku ak*tuluka panja koma panthawiyi nk*ti mozy wathawa kale moti sofiya mmene akatuluka mozy sanamupeze. Kenako sofiya anangonyamuka kumapita misozi ikusika mmasaya. Emily atasala nae anatuluka panja moses sanampeze kenako anangotolela Zinthu zake kumapita kunyumba ali okhumudwa.

Atafika Emily anazinvela ekha chisoni mumtima chifukwa amamukhulupilila mozy k*ti sangamupange zinthu ngat zimenezo. Mmawa k*tacha Emily sanachitile mwina koma kupita kwa sofiya k*ti akamufunse chomwe akafuna kupanga ndi moses. alimunjila anakumana ndi mozy koma mozy ayamuona Emily amagwesa nkhope koma emily sanaonese kukhumudwa. Atakumana anapasana moni kenako Emily anamufunsa mozy anvekele moses umandikonda? Koma mozy sanayankhe kanthu ankangomuyang'ana. Emily ataona k*ti sakuyankhidwa ananyamuka k*ti azipitiliza ulendo koma mozy anamugwila nkono nati, Emily ndikupepese chifukwa cha zimene zinachitika zulo ndipo sindikuna kukunamiza chifukwa ngati ndikunamiza zionesa ngati ine sindimakukonda pamene sizili choncho Ndipase mpata ndikuuze chilungamo kekako moses anagwada pansi mogonja naati Nditakufunsila usanandilole sofiya mdinakumana ndi sofiya ndipo anandikopa k*ti ndikhalenae pa chibwenzi poti ine ndi munthu ndimalakwa ndinakopekanae mpaka tinagwa mchikondi Emily anati.....wait part (6)

01/11/2021

(4)

πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’“πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”πŸ’”

Tinalekeza poti sofiya anatengana ndi mozy k*t akagone kunyumba kwa sofiya koma panthawiyi mk*ti Emily ali komweko. Continue πŸ‘‡

Atafika sofiya anamuuza mozy k*ti imakae panjapa mdikayale kaya pogona koma atafika pachiseko anadabwa ndi mmene anasekela. Pochoka iye anaselela kunja koma panthawiyi chiseko chimaoneka k*t changobwezedwa kusonyeza k*ti nkatimo muli munthu.
Atachikankha anamupeza Emily ali chigonele pa mphasa apatu sofiya anasowa ntengo ogwila. Mosataya nthawi anabwelela chammbuyo k*tulika panja kukamuuza mozy nati"mmm sorry mng'ono wanga wagona mkatimu ndie eeee zavuta mozy anamufunsa sofiya k*ti, ndiezingatheke tikagone kwathu koma?
Sofiya nayankha naati ayi ndibwela mawa. Kenako mozy ananyamuka ulendo kubwelela kwao.

Komatu panthawiyi imene sofiya akasegula chiseko muja Emily anali asanagone koma anangozifookesa dala k*ti aoneke ngati wagona cholinga chake amafuna aone k*ti sofiya anali k*ti mpaka kufika Usiku pakhomo koma mwayi chifukwa sofiya analowa yekha munyumba.
Moses atapita sofiya analowa nyumba kuyamba kumuzusa Emily, ndipo Emily atavomela anamufunsa sofiya naati unalik*ti nthawi zino sofiya masikwano sindikukuona bwino. Sofiya kuyankha anangoti ndinali ku trading ndie macheza anakoma. Emily anangoti ok chabwino, apatu sanakambilane zambili onse anagona. mmawa k*tacha Emily anabwelela kwao.

Patadusa week imozi Moses anakumana ndi Emily mozy anamufunsa Emily nati Bea chifukwa chani sukonda k*ti tizikumanakumana? Emily anayankha nati mozy inetu ndikuopa kupanga mistake chifukwa kungotenga mimba ndisowa kopita chifukwa makolo anga ndiovuta. Koma moses anati mmm Emily ukuganiza inendingakupase mimba kukukana Come on Bea ndimasowa nthawi yako ine ndikufuna tipite malo aphee tikasangalale kwakanthawi kochepa bas. Emily anaesa kukana koma sizinapindule kanthu. kenako mokakamizika Emily analola koma kanali koyamba k*ti apange zinthu ngati zimenezo. Mozy monga mwa chizolowezi anamutengela Emily ku room ngat mmene amapangila ndi sofiya atafika anasangalala monga pa chikondi atamaliza anabwelela kunyumba. Kuchoka panthawiyi Emily anayamba kunva moyo kukoma moti pena amachita kumuuza mozy k*ti akumufuna akakumane.
Sikulina mozy mwachizolowezi amamutenga Emily ulendo wa ku room ali komweko sofiya anamuimbila 4n mozy nati mozy ndimakufuna k*t tikambilane zinazake ndie ukandipeza ku room timakumana kuja ndasogola undipeza komweko kenako sofiya anadula 4n. wait part 5

Address

Springs

Telephone

+27655649989

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mark Chichewa sweet store's posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share