Reverien ciza

Reverien ciza Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Reverien ciza, Baby & children's clothing store, Lilongwe.

20/05/2021

```ONETSETSA KUTI MWAWELENGAKO NKHANI YOOPSAYI NDIYOPATSA CHIDWI YAMWANA WINA WAZAKA 12 YEMWE ANAGWIRA NJOKA YAMTUNDU NGATI YOMWE MUKUIONA PACHITHUZICHI.
Story witten "By Aubrey That'sDhe Boss"
Koma zoopsa ndithu, Mwana wakwaneba dzana anapita kokasaka mbewa ndi anzake, atazipeza pomwe zimalowa anayamba kukumba, zimaoneka k*ti analiko odziwa anali mwana wakwanebayu chifukwa ndiyemwe amatanganidwa ndikukumba...
Ma sign oti mbewa ziliko amawaona koma amadabwa k*ti sakuzipeza, nde amayesa kupisa nkono onse koma kumangopita osagunda kanthu, anathandizana kukumba kufikira mwana wina atapisa nkono wake anaona k*ti akugunda kanthu, mwana wakwanebayu nayenso anapisa ndipo anakuwa ndi mphamvu k*ti WAIGWIRA!!! ...
Atachotsa nkono anapeza k*t wagwira chinjoka chachikulu chomwe chidadyako mbewa zomwe zinali kuunako, mwai ndioti anaigwira pakhosi, anzake aja atamuona anathawira patali ndikumuuza k*ti
"UKANGOISIYA IKULUMA!! ", mwanayu anayamba kulira koma njoka ili m'manja,
apapa anali ataigwira ndi manja onse sopano komanso ndimphavu zake zonse...
Apa adayamba kulira uku akupita komwe kudali bambo ake, anafika kunyumba kuja akulira ndipo anangofikira kufunsa k*ti bambo anga ali k*ti, anthu mosaziwa kanthu anamuuza k*ti alikomwe amamanga nyumba koma atamuyang'ana anapeza k*ti adali ndi NJOKA m'manja mwake ndipo akulira, anthu aja anazuma koopsa ndipo anamuuzanso k*ti njoka imeneyo ndiyoopsa ukangoisiyatu ikuluma, iye sanafooke ananyamuka ulendo wakomwe kunali bambo ake...
Anthu aja anamuuza mwamuna wina yemwe anali nyumba k*ti mwana wakwaneba wagwira njoka m'manja koma akulira, bambo uja anatuluka nkumuitana k*ti abwerere koma mwana anakanitsitsa k*ti akupita kuli bambo ake, anthu nseu onse amangomuthawa kaamba koti wagwira njoka m'manja mwake yomwe idali yoopsaso kwambiri, atafika bambo ake kumuona anaseka chikhakhali ndikumuuza k*ti njoka zantundu umenewo siziluma basi iponye pasi sikuluma, mwana uja anafunsa bambo ake k*ti atsimikizedi ngati ndi choncho,
ndipo Bambo anamuuza k*ti asakaikenso,
basi ataiponya pansi anapeza k*t njoka ija inali itafa kale kaamba koti anaigwira kwambiri pakhosi ndiye imalephera kupuma...
M'menemutu ndimomwe ukukhalira moyo walero, anthu ambiri tili mumavuto akulu sitikugona kaamba kavuto lomwe tili nalo, koma kaamba ena anatiuza k*ti tchimo limenelo, zomwe tinachekera nzoopsa tikasiya kuchita zimenezo tizafa, tizasauka, mwina tizapenga misala, k*tero wina wake lero ak*tukwanidwa daily kunenedwa hule kaamba koti ali pachibwenzi ndi mwamuna wamwini, zinamutopesa koma amaona k*ti akasiyana ndi mwamuna ameneyo asauka, basi ali kakaka muzimenezo,
Ena anaputa nyanga moti amagonana ndi amai awo, amapha munthu chaka ndi chaka, kusunga zithumwa, mbiya komanso njoka koma nk*ti pano zinawatopetsa koma kaamba asing'anga anawauza k*ti ukazangosiya uzapenga basi amachitabe mantha.
"UKAISIYA IKULUMA" m'bale anthu akudziko mau awo ndikukhumudwitsa cholinga usapeze mtendere, kodi m'mene amati akaisiya imuluma amaganiza k*ti izakhala ili m'manja mwake mpaka liti, akamati mukasiya uhule muzasauka amaganiza k*ti muzapanga uhule mpaka liti, muzabera wanthu mpaka liti, muzapanga zokhwima mpaka liti, satana kwake nkuopseza chifukwa akuziwa zomwe mungapeze mutasiya zimenezo, ndinakondwera kwambiri ndi effort ya mwana uja yofuna kuuza bambo ake ataona k*ti wakumana ndi mavuto ndipo anamuthandiza zomwe sanayembekezere, vuto lanulo tamuuzeni Ambuye musiye kumangolalika paliponse, timatchimo timeneto kwa Bambo wanu wakumwamba ntosaluma, azangokuuzani titayeni pansi tilibe ntchito, iye ak*ti NDIITANE INE NTHAWI ZONSE NDIPO NDIZAKUYANKHA NDIKUKUONETSA ZAZIKULU ZOMWE SUZIZIWA.
Mwana uja sakanapeza mtendere njoka ili manja, choyamba amafunika asiye njoka ndipo anapezadi mtendere.
Naweso siya zintchito zooioazo ndipo mtendere udzaupeza.
Sungamalilire mtendere wakumwamba pomwe njoka ili m'manja.
Tiyen tilape machimo ndipo azatidalitsa ndizopambana.
Onetsetsa k*ti wamudalitsako munthu wina wake pomugailako uthengawu tsiku lalelo lino popanga share nkhani-yi at least to 3 groups komanso kwama friends anu.
WhatsApp number for group
+265994917253
&
Facebook group
https://facebook.com/groups/150396872450702
Mukhale nditsiku labwino pamene mukupanga chisakho choyenera pamoyo wanu kamba kauthengawu.
God bless your day! # Amen
Written by "Aubrey That'sDhe Boss"```

12/05/2020

Address

Lilongwe
996517217

Telephone

+265996517217

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Reverien ciza posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share