DJ TRIZA MW

DJ TRIZA MW Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from DJ TRIZA MW, Women's clothes shop, Nsanje.

30/06/2024

Mwenzi wa June towichose mu calender watha anthu kwambili mm😭

19/06/2024

Sono bwa? John ufuna chani? Unandisiya manja alinkhosiπŸ˜‚πŸ˜‚πŸ˜‚

Anayimba nyimbo imeneyi ndani Kodi?πŸ”₯🀣🀣

11/06/2024

Mafukeni amfiti nonse muchenjele paja umazitamatu k*ti ndiwe katakwe, tiwuze komwe kuli ndege πŸ˜”πŸ˜”

CHENJEZO KWA AZIMAYI NDI ATSIKANA Ndizoopsa kwambiri Masiku Otsiliza ano satana akubwera ndiuukali ndikuulusa kwambiri k...
06/06/2024

CHENJEZO KWA AZIMAYI NDI ATSIKANA

Ndizoopsa kwambiri Masiku Otsiliza ano satana akubwera ndiuukali ndikuulusa kwambiri kufuna k*tengera anthu ambiri kugahena

Choyamba ndikufuna ndikuuzeni k*ti tchimo lilironse silidzalowa kumwamba sivuto k*ti anachimwayo ndi Abusa, Alaliki, aneneri,mayi busa ayi

Azimayi ndi atsikana ambiri adzalira kwambiri patsiku lacheweruziro

Hoseya 2:2
"""Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pak*ti sali mkazi wanga, ndi Ine sindiri mwamuna wace; ndipo ACOTSE ZADAMA ZACE PANKHOPE PACE, ndi zigololo zace pakati pa maere aceβ€žβ€žβ€ž

Pa buku la Hoseya akuulura k*ti ""mkazi wina aliyense ophoda kukhope amakhala k*ti wayika zadama/zahule""

Ndinthundi aliyense ophoda kukhope amaoneka mokopa amuna ndipo amuna ambiri Ali m'uchimo losilira

Kuphoda ndi tchimo limene lik*tengera 90% la akazi ambiri kugahena

Kunena mosabisa Lero azibusa, Alaliki kapena aneneri Amene amanena k*ti kuphoda sitchimo Ali paulendo opita kugahena ngati salapa

Ambuye Yesu Ali Nanu mlandu Inu Amene mukuyikira kumbali tchimo la kuphoda

Munthu kungofa ndi tchimo lakuphoda amakafikira kugahena ngakhale umapemphela bwanji

Muntha kunyaranyaza lero koma anthu yena tchimo lakuphoda lomweli akulira nalo

LAPANI!! LAPANI!!! LAPANI!!!

SIYANI KUPHODA KUKHOPE ...
Chonde gawani uthengau kwa azanu Komanso kuma grupo omwe muli nawo

04/06/2024

Nayeso ogwiliridwa avekele sipamenepo nanu πŸ€£πŸ˜‚πŸ˜œπŸ˜œ

KADZUTSA WA MAUπŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ™1 Akorinto 1613 Khalani tcheru; khazikikani mΚΌchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu...
29/05/2024

KADZUTSA WA MAU

πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ™

1 Akorinto 16

13 Khalani tcheru; khazikikani mΚΌchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.

14 Chitani zonse mwachikondi.

mmawa wabwino ambuye akusamalileni πŸ™πŸ™

28/05/2024

Wawa mulipo anthu inu? Ngati mulipo tangonenani wawa

*MAU OKULIMBIKITSANI*PALIBE CHINSINSI PA DZIKO LAPANSILuka 12:2 Koma kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidw...
26/05/2024

*MAU OKULIMBIKITSANI*

PALIBE CHINSINSI PA DZIKO LAPANSI

Luka 12:2 Koma kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

AMEN MPINGO

Eklesia wa Mulungu anthu ena akuona ngati asunga chinsinsi anthu ena akuona ngati sizingaululike zomwe achita mwina zoipazo achita ndi iwowo koma amnamizira mzawo ndipo mzawo ali pa mavuto mwina kudwaladwala kuja ena akudziwapo kanthu mwina k*tha kwa ntchito yathu mwina kusabereka kwathu ena akudziwapo kanthu mwina kusowa banja kwathu kusakhazikika k*thaitha mikangano ya banja mwathu mwina akudziwapo kanthu mwina ana omwe tili nao si athu anthu akusunga chinsinsi koma mkuona kwao ak*t sizingadziwike koma mau a Mulungu ak*t palibe kanthu kachinsinsi pa dziko lapansi kamene sikangadziwike choncho ena tasunga zinsinsi zoipa ndimati ndikulangize k*t lapani machimo amenewo chifukwa ena mwawanamizira aja mwawathetsera banja aja mwawachotsetsa ntchito aja ndi opemphera sakugona tulo akusala kudya akukwera mapiri zidziwika zimveka mwa Ambuye

26/05/2024

Tiyeni nafe Aku south Africa tivothe NAWO APA
β–‘ DPP
β–‘MCP
β–‘UDF
β–‘UTM

Palibe chinthu chimene sichitha ayi, ngakhale nyengo zowawa zimene aliyense amangakumane nazo ilipo nthawi zidzatha ndip...
24/05/2024

Palibe chinthu chimene sichitha ayi, ngakhale nyengo zowawa zimene aliyense amangakumane nazo ilipo nthawi zidzatha ndipo adzasintha ndikuyambanso kusangalala,
(Matenda amatha)
(Umphawi umatha)
(Kusabeleka kumatha)
(Kukanidwa kumatha)
(Kusowa kwa mtendere kumathaso ndipo ndikukhala ndi mtendere)

Choncho khalani olimba muchikhulupiliro chanu, chiyembekezo chanu chisachoke pa Mulungu chifukwa Iye ndiye zonse, ndipo palibe chomwe chingamulake Mulungu.

*AMEN AND AMEN*πŸ‘πŸ‘πŸ§ŽπŸ»πŸ§ŽπŸ»πŸ§ŽπŸ»

Ndi uthenga umenewu apangileni share amzanu ndipo mulungu sakusiyani chimonzi monziπŸ™πŸ™

*πŸ“–{{TIPEMPHERE}}πŸ“–*πŸ“–πŸ™πŸ“–πŸ™πŸ“–πŸ™πŸ“–πŸ™πŸ“–*YEHOVA MULUNGU* wathu wamoyo ndi wachifundo ndinu Atate wathu wamphamvu zonse, ife ana anu t...
22/05/2024

*πŸ“–{{TIPEMPHERE}}πŸ“–*
πŸ“–πŸ™πŸ“–πŸ™πŸ“–πŸ™πŸ“–πŸ™πŸ“–
*YEHOVA MULUNGU* wathu wamoyo ndi wachifundo ndinu Atate wathu wamphamvu zonse, ife ana anu tikudza mogonja ndi modzichepetsa kumpando wanu wachifumu munthawi ino yammawa pofuna kupeleka ulemu komanso matamando kwainu mfumu yacholengedwa chonse inu mukure ife tichepe, Zikomo chifukwa mwatipatsanso mwayi owonjezera tsiku ili lokhara ndimoyo pano padziko lapansi, Inu mulemekeze mutamandike kunthawi zonse chifukwa chazimene mwatipangirazi mosawerengera mphulupuru komanso zochimwa zathu.

*AMBUYE MULUNGU* Wosamara ndik*teteza ndinu, ndipo tikupempha chitetezo chanu pamiyoyo yathu pak*ti mdyerekezi ndi ziwanda zake wakonza maplani oipa k*ti atitsamwitse, koma mudzina lamphamvu lamwana wanu Yesu khrist Mulungu wamoyo, maplan onse awoyipayo akhare wolephereka pamene tikuyamba week yimenei chilichonse chikhale chotheka pak*ti mwini zonse ndinu nkhawa zathu zonse titulira painu Ambuye inu mukure ife tichepe, kumbukirani wodwala wonse ndipo iwo akachilitsidwe wonse ali paulendo muwa tsogolele ndinu Baba tathokoza komanso kukupemphani zonsezi kudzera mudzina lamphamvu lamwana wanu Yesu mpulumutsi wathu wamoyo tapemphera,

*πŸ“–AMEEENπŸ“–πŸ™πŸ™.*

*_YEHOVA AKUFUNA K*T TIKHALE ANTHU OKONDANA_* πŸŒΎπŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸŒΎ *Aroma 12:9-12* { _Makhalidwe okoma otiyenera._ } 9 Cikondano cikh...
20/05/2024

*_YEHOVA AKUFUNA K*T TIKHALE ANTHU OKONDANA_*
πŸŒΎπŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸ“–πŸŒΎ
*Aroma 12:9-12*
{ _Makhalidwe okoma otiyenera._ }

9 Cikondano cikhale copanda cinyengo.
Dana naco coipa; gwirizana naco cabwino.

10 M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;

11 musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

12 kondwerani m'ciyembekezo piriranim'masautso; limbikani cilimbikire m'kupemphera.

*Hallelujah Hallelujah*

Okondedwa umu ndi mmene Yehova Afunira Ak*ti tikhale anthu Okondana Pakati pa wina ndi mnzace tidane ndi zoipa koma tiyanjane ndi zabwino kotero umu ndi momwe Yehova Afunira Ambuye Akudalitsen ngat mumakwaniritsa izi koma ngat simunachitepo Yamban Lero Kukonda mzanu Monga muzikondera Inu Mwini Kumwamba Kulandire Ulemu Nthawi zonse. πŸ‘πŸ‘πŸ‘

Ndi uthenga umenewu apangilekoni share amzanu ndipo mulungu sakusiyani chimonzi monzi

Address

Nsanje

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when DJ TRIZA MW posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share