10/05/2026
Zaka zoposa 16 zapitazo, munthu wina anasiya mwana wa miyezi pafupifupi 7 pa khomo la nyumba yathu. Wantchito wathu wam’nyumba ndiye anayamba kuona mwanayo ndipo anathamanga kudzatiwuza.
Tonse tinadabwa kwambiri. Sitinangomusunga nthawi yomweyo ayi. Tinakhala miyezi yoposa 9 tikufufuza makolo ake enieni. Ndithu, tinachita chilichonse… kulengeza pa wayilesi, misonkhano ya m’dera, mpaka kupita ku polisi. Koma palibe amene anabwera kudzamutenga. Sitinkafuna kuti akakulire ku malo osungira ana amasiye. Choncho, tinaganiza zomulera mwalamulo ngakhale kuti tinali kale ndi ana awiri athu. Anakhala mwana wathu wachitatu.
Anakulira limodzi ngati abale ake ndipo sitinamusiyanitsepo ndi ana athu obadwa nawo. Timamukonda ndi mtima wonse, ndipo wakhala mbali ya banja lathu kwa zaka zoposa 16.
Chinthu chovuta ndi chakuti tsopano mwanayo ali pafupi kumaliza sekondale ndipo pafupifupi zaka 17 kuchokera pamene tinamulera, mayi ake omubala awonekera mwadzidzidzi kuchokera kosadziwika kudzamutenga.
Kwa ma week atatu tsopano, mkaziyu wakhala akumenyana nafe chifukwa cha mwanayo, akufunafuna kuti timupereke. Akuti ali wokonzeka kuchita DNA kutsimikizira kuti mwanayo ndi wake. Tsiku lililonse amabwera kunyumba kwathu kulira. Anabweretsanso m’busa wake kudzapempha kuti timupereke mwanayo.
M’mawa uno, anabweranso ndi m’busa wake ndipo anafika patali. Anaopseza kuti adzadzivulaza ngati sitibwezera mwanayo mkati mwa ma week awili . Anatinso ngati china chilichonse chingamuchitikire, magazi ake adzakhala pa manja athu.
Ine ndi mwamuna wanga tili okhumudwa kwambiri. Kodi mungasiye bwanji mwana amene mwakhala naye, kumukonda ndi kumulera kwa zaka pafupifupi 17? Tili pa chisokonezo chachikulu ndipo sitikudziwa choti tichite. Zikutipweteka kwambiri komanso kutisokoneza mtima 💔😥🤦” tinthandizeni abale tipange bwanji .tithandizeni maganizo anu